21/06/2026
‼️NBS Bank donates ZAR 420,000 to repatriate 140 Malawians caught in SA xenophobic attacks ‼️
At NBS Bank, officials say caring goes beyond banking. The bank announced it has contributed ZAR 420,000 to fund the safe return of 140 Malawians affected by recent xenophobic attacks in South Africa. The initiative aims to reunite the victims with their families and loved ones back home.
“As one people, we have a shared responsibility to care for one another in times of need,” NBS Bank said in a statement released Friday. The bank described its donation as part of a broader commitment to community welfare during humanitarian crises.
NBS Bank is now calling on other organisations, businesses, and well-wishers to join the effort. “We invite everyone to be part of this noble cause as we work together to bring our fellow Malawians home safely,” the statement added.
The bank reiterated its belief that unity in hardship strengthens the nation. “Because caring for one another is what makes us stronger as a nation,” it said.
‼️ CHICHEWA‼️
Ku NBS Bank, akuluakulu akuti kusamalira kumapyzola ntchito zamabanki. Banki yalengeza kuti yapereka ZAR 420,000 (pafupifupi MWK44.3 million ) kuti ithandizire kubweretsa kunyumba aMalawi osachepela 140 motetezeka omwe akhudzidwa ndi ziwawa zosankhana mitundu zomwe zikuchitika ku South Africa. Ntchitoyi ikufuna kugwirizanitsanso anthuwo ndi mabanja awo komanso okondedwa awo kwawo.
"Monga anthu amodzi, tili ndi udindo ogawana komanso wosamalirana wina ndi mnzake pa nthawi yamavuto,” inatero NBS Bank m'mawu omwe adatulutsa Lachisanu. Banki idalongosola kuti chopereka chake ndi gawo la kudzipereka kwakukulu ku ubwino wa anthu ammudzi pa nthawi yamavuto.
NBS Bank tsopano ikuyitanitsa mabungwe ena, mabizinesi, ndi othandizira onse kuti alowe nawo mu ntchito imeneyi. “Tikuitana aliyense kuti atenge nawo gawo pa ntchito yabwinoyi ndipo tigwirire ntchito limodzi kubweretsa abale athu aku Malawi kunyumba motetezeka,” anawonjezera akuluakulu a bankiyi.
Banki idabwerezanso kuti chikhulupiriro chake ndichakuti umodzi pa nthawi yamavuto umalimbitsa mtundu. “Chifukwa kusamalirana wina ndi mnzake ndi zomwe zimatipangitsa kukhala olimba monga mtundu,” anatero akuluakulu a banki ya Nbs.
# #